مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه

CHOMBO CHACHIPULUMUTSO

Cover Page
By

Sheikh Salim bin Samayr al-Hadrami

مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 1 · Introduction Yoyamba
⏱️ 20:57
“Kudziwa zokhudza buku li:” Buku li likufotokoza zokhudza ma ibadaat osiyana siyana. Mulibe ma aamalaat ngati zokhudza nikkah, jihaad ndi zina kudzera madh'hab (panjira) ya Imam a Shafi.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 2 · Introduction ya chiwiri
⏱️ 31:24
“Kumulongosola Mulembi:” Introduction ya chiwiri, ikufotokoza zokhudza mulembi, mbiri yake. Uku kukhala kumaliza مقدم (introduction) ya buku li. Izi zimathandiza kwambiri kudziwa bwino zokhudza zomwe zinalembedwa mu book.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 3 · Kudziwa Madhhab ndi Msichi za Chisilamu
⏱️ 32:48
Sheikh anayamba ndikutitambasulira zokhudza madh'hab. Madh'hab si chipembedzo kapena mpingo. Madh'hab ndi njira yomwe ma ُعُلَمَاء (scholars) amagwilitsa tchito kufokotokoza chipembedzo, kuti anthu avetsetse chipembedzo. Kutero sizoletsedwa kwa msilamu kuphuzira madh'hab enaake. Koma kuti, madh'hab safunika kuwatsatira mwa umbuli kufika pomatsutsa Qur'an ndi ma hadith a swahih kamba kotsatira madh'hab.
مَنْ يُرِدِ اللّٰهُ بِهِ خَيْراً يُفَقِّهْهُ فِي الدِّينِ (Amene Allah angamufunire zabwino, amampatsa kunvetsa chipembedzo). Zili zabwino kwa msilamu kuti akamayamba zinazake adziyamba ndikumuyamika Allah. Izi sitikuyenera kumazipanga ku zithu za deen zokha iyayi, ngakhale za duniyah zimafunika kumampempha chithandizo Allah (سبحانه وتعالى) kuti zitiyendere bwino.
Sheikh, anayamba ndi kutipatsira khomo la msichi za Chisilamu (ِأَرْكَانُ الْإِسْلَام). China chilichonse chokhudza Chisilamu chinagona kapena Kutuluka mu msichi 5 zomwe ndi ku: 1. Kukhulupira kuti palibe wina oyenera kupembedzedwa koma Allah ekha komanso Muhammad ndi Mtumiki wa Allah. 2. Kuimika swalah 3. Kupereka zakah 4. Kusala mmwezi wa Ramadhan 5. Kupita ku Hajj kwa amene Allah wamufewetsera
Asilamu tiyeni tiphunzire kuti tidziwe komanso kuvetsetsa chipembedzo chi. Izi zithandiza kubweretsa umodzi pakati pathu.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 4 · Msichi za Iman
⏱️ 25:16
“Msichi za chikhulupiliro (Imaan), ِأَرْكَانُ الْإِيْمَان:” Msichi za Chisilamu ndizosiyana ndi msichi za imaan. Asilamu, dziwani kuti ngati munthu angapange kapena kukwanilitsa msichi za Chisilamu opanda imaan, zikhalama zopanda zipatso.
Msichi za imaan zilipo 6 Kukhulupilira mwa; 1. Allah 2. Angelo ake 3. Mmabuku ake 4. Atumiki ake 5. Tsiku lomaliza 6. Mu mchikozero chabwino komanso choyipa zimachokera kwa Iye, Allah
Tinaonaso gawo la tathauzo la tauhid. Tauhid ndi kukhulupilira kuti palibe wina opembedzedwa mwa choonadi koma Allah ekha basi, لَا إِلٰهَ إِلَّا اللّٰهُ. Tiyenera Kudziwa kuti, kuti tipindure ndi لَا إِلٰهَ إِلَّا اللّٰهُ, tiyenera kudziwa bwino bwino zokhudza mawu amenewa. Koma ngati tingapange chidule ponyalanyaza kudziwa kapena kuphuzira tathauzo lake, ndithu tidzakhala osochera ndi otayika. Asilamu ambiri ngati akupanga zinthu molakwika ndi kamba koti sananvetse bwino tathauzo la لَا إِلٰهَ إِلَّا اللّٰهُ. Allah atiteteze kuzimenezi.
Munthu ayenera kudziwa ndi kutsimikiza zoti palibe wina opembedzedwa koma Allah ekha kuyambira mumtima mwake, kenako alakhule ndi lilime lake ndipo ziwalo zake zitsatire pogwira tchito yopembedza Allah ekha yo basi.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 5 · Zizindikiro za kutha Msikhu
⏱️ 36:06
“Zizindikiro zakutha msinkhu, عَلَامَاتُ الْبُلُوغِ.:” Ndi zofunika kuti msilamu adziwe zizindikiro za kutha msinkhu chifukwa malumulo a Chisilamu amayamba kugwira tchito pa munthu pamene wakula. Mtumiki anati: "رُفِعَ الْقَلَمُ عَنْ ثَلَاثَةِ ", tathauzo: "Cholembera chimanyamulidwa kwa anthu atatu". Kutathauza kuti Angelo samalemba machimo a anthu atatu. Mmodzi mwa iwo ndi mwana mpaka atatha msinkhu, ْعَن الصَّبِيِّ حَتَّى يَحْتَلِمَ.
Zizindikiro zakutha msinkhu zilipo zitatu: 1. Kukwanitsa zaka 15 2. Kudzilotera kwa munthu amene wafika zaka 9 3. Kusamba kwa munthu wa mkazi amene wafika zaka 9
Tikamakamba za mthawi ku sharia (malumulo a Chisilamu), timagwiritsa tchito hijri calendar (ya Chisilamu) chifukwa imasiyana ndi Gregorian calendar (Yomwe timagwiritsa tchito kwathu kuno).
Komanso tidziwe kuti zizindikiro zi sizikufunika kuti zonse zikumane pakamodzi. Kupezeka kwa chimodzi mwa zizindikiro zimenezi kumakwanira kuti mwana watha msinkhu, wakula.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 6 · Kupeza twahara pogwiritsa tchito mwala
⏱️ 33:42
“Kugwiritsa tchito mwala, tissue ndi zina podziyeretsa, ُالْاِسْتِنْجَاء:” Kudziwa mmene tikuyenerera kudziyeretsera ndi zofunika kwambiri kwa Msilamu chifukwa pali zinthu zina ngati swalah komanso ma ِعِبَادَات ena omwe tikuyenera kupanga tili ndi twahara, oyera.
Sheikh anatidziwitsa za malamulo amene amayenereza kugwiritsa tchito mwala popanga istin'jaai, ُالْإِسْتِنْجَاء. Istin'jaa, njira yochotsera nyasi pogwiritsa tchito madzi, ndi njira yoyamba yodziyeretsera, first priority. Pamene Istijmaar, njira yochotsera nyasi pogwiritsa tchito mwala ndi zina zolowa mmalo mwa mwala, ndi njira ina yodziyeretsera, second priority.
Njira yogwiritsa tchito mwala, inabwera kamba kofuna kupeputsa chipembedzo ndipo ndi yokwanira payokha posagwiritsanso tchito madzi pambuyo pogwiritsa tchito mwala. Komanso, mwala kapena zolowa mmalo mwake zikhoza kugwiritsidwa tchito angakhale madzi alipo. Zinthu zomwe ndi najsi kapena zili ndi najsi sizoyenera kugwiritsidwa tchito podziyeretsa.
Zinthu zimene zingagwiritsidwe tchito ngati mwala pochotsera nyasi, ُنَجْس, zikuyenera kukhala ndi zithu 4: 1. Chikhale chowuma, chosanyowa 2. Chikhale cha twahara, choyera 3. Chikhale ndikhuthekera kochotsa najsi 4. Chisakhale chinthu cholemekezeka
Tidziwe kuti kusowekera kwa chinthu chimodzi mu zinthu zoyenereza kugwiritsa tchito mwala pochotsa nyasi, kumampangitsa munthu kuti abwerere kogwiritsa tchito madzi.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 7 · Malamulo amene amayenereza kugwiritsa tchito mwala
⏱️ 30:50
“Malamulo amene amayenereza kugwiritsa tchito mwala popanga istinjaa, ِشُرُوطُ إِجْرَاء الْحَجَرِ فِي الْاِسْتِنْجَاءِ:” Ndizofunikira kuti tidziwe kuti instijaa ili ndi malamulo ake okwana 5: 1. Zokakamiza munthu kupanga istinjaa 2. Zabwino kukapanga istinjaa 3. Zololezedwa chabe kukapanga istinjaa 4. Zonyasa kukapanga istinjaa 5. Zoletsedwa kukapanga istinjaa
Najsi (نَجْسُ) ndi nyasi kapena chilichonse cha unve. Malumulo amene amayenereza kugwiritsa tchito mwala popanga istinjaa alipo 8: 1. Ikuyenera kukhala miyala itatu 2. Miyalayo kapena cholowa mmalo mwa mwala chikuyenera kukhala ndi kuthekera kuchotsa najsi 3. Najsi sikuyenera kukhala yowuma 4. Najsi sikuyenera kusamuka ndi kugunda mbali ina yathupi 5. Sipakuyenera kubwera najsi ina pamwamba pa najsi yo 6. Najsi sikuyenera kuyenderera mpaka kugunda mmatako 7. Najsi yo isagundindwe ndi madzi 8. Miyala yopangira istinjaa ikhale yoyera
Tidziwe kuti, kusowekera kwa chimodzi mwa izi, mzimakhala zokamazikika kuti munthu agwiritse tchito madzi pochotsa najsi.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 8 · Zikakamizo za pa wudhu
⏱️ 33:14
“zinthu zichikakamizo popanga wudhu, ِفَرَائِضُ الْوُضُوْء:” Ma عُلَمَاءُ, scholars, a madh'hab a Shafi anaugawa wudhu mu ma gawo awiri; 1. Zinthu zachikakamizo pa wudhu 2. Zinthu zomwe zili sunnah pa wudhu
Tidziweso kuti kavedwe komati pali wudhu wa فَرَضٌ (wachikakamizo) ndi wa سُنَّةٌ (sunnah) ndi kolakwika chifukwa, zimatathauza kuti ngati tingasiye osapanga wudhu wa chikakamizo ndeti wudhu wathu sunatheke.
Zinthu zimene zili zachikakamizo kupanga pa wudhu zilipo 6: 1. Chitsimikizo النِّيَةُ 2. Kusambitsa kukhope 3. Kusambitsa mmanja awiri mpaka mkasukusuku 4. Kupukuta pa mutu 5. Kusambitsa miyendo iwiri 6. Kupanga mwa ndondomeko التَّرْتِيبُ
Asilamu tidziwe kuti wudhu ndi chinthu chofunikira kwambiri chifukwa ndi chinthu chimodzi chomwe chimafufuta machimo a munthu wopanga yo komanso ndi chitetezo ku zinthu zonyasa monga ziwanda (ma jinn). Ngati tingapange wudhu mosasamala komanso mwa umbuli ndeti sitidzapeza ma phindu ake komanso tidzakhala ndi chilango.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 9 · Kufokotokoza za wudhu, chitsimikizo ndi ndondomeko
⏱️ 26:19
“Kupitiliza kufokotokozera wudhu:” Tikumbutsane kuti paja buku lomwe tikuphuzitsana li, linalembedwa ndi Madh'hab a Shaffie. Kumbali ya wudhu, madh'hab Shaffie anawugawa wudhu mmagawo awiri amene tinabweretsa mu lesson 8 aja kuti; "Zinthu zachikakamizo pa wudhu" ndi "Zinthu za sunnah pa wudhu". Komanso anatibweretsera zithu 6 zomwe zili zachikakamizo pa wudhu. Kutathauza kuti zinthu zomwe sanazibweretse mu zinthu 6 zi, madh'hab a Shaffie anazitenga kuti ndiza Sunnah, monga;
  • Kutsuka mkamwa ndi mphuno, المضمضة و الاستنشاق.
  • Kusambitsa kepena kutsuka ziwalo katatu
  • Kupukuta mmakutu

Kutengera kuti maphunziro anthu sali limited ku za madh'hab a modzi komanso kukana kutsatira madh'hab mwa umbuli. Madh'hab ena komanso ma عُلَمَاءُ (scholars) ena, samawugawa wudhu mmagawo awiri. Kutathauza kuti amangoika kuti wudhu ndi umodzi basi kutengera ndi ma umboni ochokera kwa Mtumiki wathu (ﷺ) kuti sanawugawe wudhu mmagawo awiriwa komanso sanasiyeko osatsuka mkamwa ndi mphuno ndi kupukuta pa mmakutu.
Madh'hab ena ndi ma Ulamaa anawunikiranso kuti pamene Allah watilamula kusukusula ku maso (فَاغْسِلُوا وُجُوهَكُمْ), nkhope singakhale nkhope opanda pakamwa ndi mphuno. Kutathauza kuti pakamwa ndi mphuno ndi mbali imodzi ya nkhope. Chimodzimodzi, kupukuta makutu zili pamodzi ndi kupukuta pa mutu, وَامْسَحُوا بِرُءُوسِكُمْ, chifukwa makutu ndi mbali imodzi ya mutu.
Pa chifukwa ichi, zabwino kwambiri ndi kusawugawa wudhu mmagawo awiri. Izi ndi zomwe zili chifupi ndi chilungamo.
“Kupitiliza kufokotokozera wudhu kumbali ya Chitsimikizo ndi ndondomeko, ِفِي النِّيَّة وَالتَّرْتِيبِ:” Chitsimikizo (النِّيَّةُ) ndi kutsimikiza kulikonse pofuna kupanga chinthu. Munthu utha kupanga niyyah mthawi ina iliyonse potengera kufotokoza kwa ma ulama pa zomwe zili chifupi ndi chilungamo. Niyyah malo ake ndi mumtima, مَحَلُّهَا الْقَلْبُ, chifukwa mtima ndi omwe umasiyanitsa zinthu pakati popanga zinthu mwa chikhalidwe ndi kupembedza, عَادَ وَعِبَادَة. Choncho ndizosayenera kulakhula niyyah ndi lilime pomwe tikufuna kupanga tchito yopembedza ina iliyonse. Izi ndi zomwe zili chifupi ndi chilungamo chifukwa ma عُلَمَاءُ ena anati "التَّلَفُّظُ بِهَا بِدْعَة", kuyiyakhula niyyah ndi lilime ndizopeka.
Kulondoloza popanga wudhu, التَّرْتِيْبُ, kumathauza kuti kuyambira kumaso, kenako mmanja, kenako pa mutu ndikumalizira miyendo. Choncho sizoyenera kuyamba kusambitsa miyendo kapena manja usanasukusule kumaso.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 10 · Mu malamulo a madzi
⏱️ 30:44
“Gawo la mu malamulo a madzi, فِي أَحْكَامِ الْمَاءِ:” Kudziwa za madzi ndi chinthu chofunika chifukwa madzi ndi chinthu chimodzi chomwe timagwiritsa tchito kupezera twahara.
Mulembi anatidziwitsa za madzi kudzera mmagulu awiri, Madzi ochepa ndi ochuluka, الْمَاءُ قَلِيلٌ وَكَثِيرٌ. Madzi amawonengeka twahara yake pa kusintha mu zinthu zitatu; 1. Fungo, رِيحٌ 2. Mtundu, لَوْنٌ 3. Taste, طَعْمٌ
Madzi ochepa ndi omwe sanafike 200 liters, قُلَّتَينِ. Madzi ochepa amakhala a najsi ngati mwagwera najsi angakhale madziwo sanasinthe mu zithu zitatu zi.
Madzi ambiri ndi omwe adutsa 200 liters. Madzi ambiri samawonongeka twahara yake ndi kugweramo najsi kungopatula ngati atasintha mtundu, fungo, ndi taste yake.
Izi ndi zomwe mulembi anatipatsira zokhudza madzi kudzera pa madh'hab a Imam Shafi.
Mtumiki (ﷺ), anati: "إِنَّ الْمَاءَ طَهُورٌ لَا يُنَجِّسُهُ شَيْءٌ", tathauzo: "Ndithu madzi ndi oyera ndipo palibe chomwe chingawaipitse". Ma ulama anatambasula kuvetsetsa izi kuti madzi ngati anali a bwinobwino samakhala a najsi, ochepa olo ochuluka, kungopatula ngati mutagwera najsi yomwe ingasinthe mtundu, fungo, ndi taste ya madziwo. هَذَا قَرِيبُ مِنَ الْصِدْقِ, Izi ndi zomwe zili chifupi ndi chilungamo.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 11 · Zomwe zimapangitsa kusamba kukhala kokakamizika pa munthu
⏱️ 35:04
“Gawo la zinthu zimene zimapangitsa kuti kusamba kukhale kokakamizika pa munthu, فِي مُوجِبَاتِ الْغُسْلِ:” Zinthu zimene zimapangitsa kusamba kukhala kokakamizika pa munthu zilipo 6: 1. Kugundana kwa maliseche awiri 2. Kutulutsa ma niyyee, uli mtulo kapena manso 3. Kusamba (menstruation period); zimakhala zokakamikiza pa mzimayi kukasamba pamene magazi a haidhu aduka. 4. Mtayo; Zimakhala zokakamikiza pa mzimayi kusamba pamene magazi a mtayo aduka. 5. Kubereka; Zimakhalanso zokakamikiza pa zimayi kusamba pamene magazi amene mzimayi amatulutsa pambuyo pobereka aduka. 6. fa; Ndi zokakamikiza kusambitsa maliro.
Magazi amene mzimayi amatulutsa akamaliza period, الْإِسْتِحَاضَةٌ, samapangitsa kusamba kukhala kokakamizika pa iye koma amangodula wudhu. Ngati mzimayi akupanga haidhu mpaka kufika masiku 15, ameyera kusamba ndi kuyamba kuswali komanso kupanga zomwe zimakhala haram akakhala mu nyengo ya haidhu.
Zimakhalanso zokakamikiza pa mzimayi kusamba pamene wabereka koma sanatulutse magazi, ndi kuyamba kupanga zomwe zimakhala haram akakhala mu nyengo ya mtayo kapena kubereka, النِّفَاسُ وَالْوِلَادَةُ.
Mongowonjozera, kusamba kosambitsa maliro timasambitsa chifukwa cha ukhondo, kusiyana ndi kusamba kwa zifukwa zina 5 zina zija timasamba chifukwa chofuna kupeza twahara.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 12 · Mu Zikakamizo za posamba | Malumulo amene amapangitsa wudhu kukhala wokwanira
⏱️ 34:10
“Gawo la zikakamizo za posamba, فِي فُرُوضِ الْغُسْلِ:” Zomwe zili zachikakamizo posamba, kutathauza kuti zikapangidwa zimenezi kusamba kumakhala kuti kwakwanira, zilipo ziwiri; 1. Chitsimikizo, النّيَّةٌ 2. Kukwanirana kwa madzi pa thupi lonse kuchokera kumutu mpaka mmapazi
Kusamba kumene munthu angasambe ngati mmene Mtumiki ﷺ amachitira pamene ali mu nyengo yokakamizika kusamba ndi kwabwino kwambiri. عَنْ مَيْمُونَةَ، أَنَّ النَّبِيَّ ﷺ اغْتَسَلَ مِنَ الْجَنَابَةِ، فَغَسَلَ فَرْجَهُ بِيَدِهِ، ثُمَّ دَلَكَ بِهَا الْحَائِطَ ثُمَّ غَسَلَهَا، ثُمَّ تَوَضَّأَ وُضُوءَهُ لِلصَّلاَةِ، فَلَمَّا فَرَغَ مِنْ غُسْلِهِ غَسَلَ رِجْلَيْهِ‏. Hadith ikuchokera kwa Maimuna kuti Mtumiki ﷺ akakhala ndi janaba amayamba kusambitsa maliseche ake, kenako amasambitsaso manja ake, kenako amapanga wudhu ngati wa swalah, kenako amadzisambitsa mthupi lonse ndipo akamaliza kudzisambitsa amasambitsa mapazi ake.
Ngati tingasambe chonchi, zimakhala zokwanira kwa ife ku kaswali osapanganso wudhu. Chifukwa wudhu umene timapanga posamba ndiwokwanira chifukwa palibe umboni umene ukuonetsera kuti Mtumiki ﷺ amapanganso wudhu wina kuti aswali.
Mongowonjozera, "كُنْتُ أَغْتَسِلُ أَنَا وَالنَّبِيُّ، ﷺ مِنْ إِنَاءٍ وَاحِدٍ تَخْتَلِفُ أَيْدِينَا فِيهِ" Aisha akuti amasambira limodzi ndi Mtumiki kugwiritsa tchito mosambira mmodzi (Chitini or Beseni). Ndipo mmanja ake ndi a Mtumiki ﷺ amasithana mosambiramo, (Kutathauza kuti wina amati akapisa nkutunga winanso amadzapanga). Izi zikutionetsera kuti kupisa ndi manja anthu mmadzi omwe tikusamba ndi zabwino bwino. Ndi zovetsa chisoni kuti anthu ena mpakana pano samadziwa kuti kupisilira madzi osamba kulibe vuto.
“Gawo la mu malamulo amene amapangitsa kuti wudhu ukhale okwanira, فَصْلٌ فِي شَرَائِطِ الْوُضُوءِ:” Malamulo amenewa amagwiritsidwanso tchito posamba. Madh'hab a Shafi anagawa malamulo amenewa kuti alipo 10. Tinayamba ndikuwona malamulo 5 okha omwe ndi; 1. Chisilamu; Opanga wudhu yo akhale msilamu. 2. Akhale munthu oti amadziwa kusiyanitsa zinthu. 3. Akhale oyera ku unve waukulu ngati haidhu ndi kubereka or mtayo. Mwachidule, munthu yo asakhale mu nyengo zomwe zimapangitsa kuti kupanga wudhu kusakhale kolandilidwa pa iye. 4. Akhaleso oyera ku chilichonse chomwe chingalepheretse kuti madzi afike pa thupi or pa khungu lake. Umu mukulowanso zinthu zina zomwe anthu amatha kuika pa thupi, zomwe zimalepheletsa kuti madzi afike pa thupi. 5. Pasapezeke pa chiwalo chosambitsidwa chinthu chomwe chingathe kusintha madziwo.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 13 · Mu malamulo amene amapangitsa kuti wudhu ukhale wokwanira
⏱️ 30:44
“Kupitiliza malamulo amene amapangitsa kuti wudhu ukhale okwanira, شَرَائِطُ الْوُضُوءِ:” 6. Kukhala ndi uzindikiri wa chikakamizo cha kupanga wudhu ko. 7. Kuzindikira zomwe ndi za chikakamizo popanga wudhu ndi kusakhulupirira kuti ndi za sunnah. 8. Madzi adzikhala oyera, a twahara. Oyera pawokha komanso ukhoza kuyeletsera zithu zina. 9. Adzipanga wudhu mthawi ya swalah ikalowa. Lamulo ili limakhudza gulu la anthu amene amakhala ndi litsiro lopitilira. Ngati kudutsitsa masiku a haidhu ndi kubereka. 10. Kupanga molondoloza komanso mosadutsa mthawi yayitali usanasambitse chiwalo china. Komanso anthu amene amakhala ndi mavuto a litsilo lopitilira, safunika padzipita mthawi yayitali asanaswali pambuyo poti apanga wudhu.
Lamulo lina lomwe madh'hab a Shafi samaliyang'ana ndi kuchotsa kaye najsi pathupi tisanapange wudhu, إِزَالَةُ النَّجَاسَة. Ndizofunika kuti tidzichotsa kaye najsi pa thupi tisanapange wudhu ngati pathupipo pali najsi.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 14 · Zinthu zimene zimawononga wudhu
⏱️ 34:04
“Gawo la zinthu zimene zimadula wudhu, نَوَاقِضُ الْوُضُوءِ:” Mulembi anatipatsira zinthu zomwe zimawononga wudhu wa munthu kutengera mma gawo 4 omwe anazigawira ku madh'hab a Shafi; 1. Chotuluka chilichonse chimene chimatuluka mmaliseche awiri, kutsogolo kapena kumbuyo, ngati mpweya kapena zina kupatula maniyye. 2. Kuchoka kwa nzelu zosiyanitsa zinthu kudzera mutulo kapena zina, ngati kukomoka, kupenga misala. 3. Kugundana kwa matupi a munthu wa mmuna ndi wamkazi akuluakulu omwe akhoza kukwatilana popanda chotchinga. Madh'hab ena amati izi sizimadula wudhu chifukwa Mtumiki ﷺ amatha kugundana ndi azikaze ake ali ndi wudhu koma samapangaso wudhu wina kuti aswali. Izi ndi zomwe zili kufupi ndi chilungamo. 4. Kukhudza maliseche akutsogolo ndi mkati mwa dzanja. Ma ulama ena amati kugunda maliseche kwa chilakolako kapena kugunda kwa cholinga ngati kuwaseweretsa, ndi kumene kumadula wudhu. Izi ndi zomwe zili chifupi ndi chilungamo.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 15 · Zomwe ndi zoletsedwa kwa munthu amene ali ndi umve
⏱️ 33:33
“zomwe zili zoletsedwa kwa munthu amene ali ndi umve, فِيمَا يَحْرُمُ عَلَي الْمُحْدِثِ:” Mulembi anafotokozera za unve powugawa mma gawo atatu.
1 - KUDUKA WUDHU Zimaletsedwa kuchita zinthu zokwanira 4 kwa munthu amene wudhu wake waduka;
  • Swalah
  • Kupanga tawaf (kuzungulira ka'abah)
  • Kukhudza Qur'an mus'haf ndi zikhato
  • Kunyamula mus'haf ya Qur'an

Mus'haf ndi physical Qur'an kapena Qur'an yomwe inaprintidwa mu Arabic yokha yokha. Umu mmalowamo Qur'an yonse, or Juz, or page imodzi or angapo.
Ndipo mukutulukamo Qur'an ya phone, ya pa internet, ya mma hadith, Qur'an yomwe yatathawulizilidwa mu mchiyankhulo china, kapena tafseer ya Qur'an angakhale itakhala mu Arabic. Sizili haram kugwira zimenezi chifukwa zimenezi si ma mus'haf. Izi ndi zomwe zili chifupi ndi chilungamo.
2 - KWA AMENE ALI NDI JANABA Pali zinthu 6 zomwe zili haram kwa munthu amene ali ndi janaba.
  • Swalah, tawaf, kukhudza Mus'haf ndi Kuyinyamula
  • Kukhazikika mu mzikiti
  • Kuwerenga Qur'an moti lilime lidzigwedera mwa njira ina iliyonse ngati yapamtima

3 - KWA AMENE ALI MU HAIDHU OR KUBEREKA Zili zoletsedwa zinthu 10 kwa munthu amene ali mu haidhu or mtayo.
  • Swalah, tawaf, kukhudza Mus'haf ndi Kuyinyamula, Kukhazikika mu mzikiti
  • Kuwerenga Qur'an; Ma ulama ena amati izi palibe umboni wokhazikika omwe ukuletsa mzimayi kuwerenga Qur'an ali mu mnyengo ya haidhu or kubereka. Choncho zomwe zili chifupi ndi chilungamo ndi zoti sizili haram kuwerenga Qur'an kwa mzimayi amene ali mu nyengo yake.
  • Kusala kudya
  • Kuthetsa banja; Kungopatula kuthetsa banja ngati koti "mkazi ndi mwamuna amene apanga nikkah koma sanakhale malo amodzi", kepana "mkazi akakhala oyembekezera", kapena "mzimayi kuthetsa banja".
  • Kudutsa mu mzikiti ngati akuopa kunyasitsa mu mzikiti mo; Kungopatula ngati ali pa hajja ya zofunikira kupanga or kutenga mu mzikiti mo.
  • Kusangalala naye mkazi pa zomwe zili pakati pa mchombo ndi mabondo. Kumawauza abambo adzipewa izi.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 16 · Mu zifukwa zopangira tayammum
⏱️ 26:23
“Gawo la zifukwa zopangira Tayammamu (Wudhu omwe timapanga pogwiritsa tchito mchenga), فِي أَسْبَابِ التَّيَمُّمِ:” Zifukwa zomwe zimapangitsa kuti munthu apange tayammamu zilipo zitatu; 1. Kusowa kwa madzi 2. Matenda 3. Kusawukira kwa madzi chifukwa cha ludzu ndi zinthu zina pa zinyama ndi anthu olemezeka.
Ngati madzi asowa pamalo pomwe tili ndipo pali kufunikira kuti tipange wudhu ngati kuti kuswali, Allah analamula kuti tidzipanga tayammamu. Munthawi ya matenda, ngati kugwiritsa tchito madzi kungapangitse matenda kukula kapena mthawi yochira kutalika, tili oyenera kuti tipange tayammamu. Mwachitsanzo, ngati munthu anavulala pa mkono nde akagwiritsa tchito madzi atsutsula bala lakelo ndi kupereka vuto lina, munthu ali ololedwa kupanga tayammamu. Munyengoso yozizira kwambiri yoti kugwiritsa tchito madzi wozizira kupereka vuto, tikhoza kupanga tayammamu.
Ngati madzi alipo ochepa koma akufunikira pa zinthu zina zomwe zili zofunikira ngati kuphikira komanso ludzu ku zamoyo zolemezeka, tikhoza kupanga tayammamu.
Magulu 6 a anthu ndi zinthu zomwe ndi zosalemekeza ndi;
  • Munthu amene amasiya swalah
  • Munthu wa chiwerewere
  • Munthu amene anatuluka Chisilamu
  • Kaafir
  • Galu wachiwewe
  • Nkhumba

Munthu amene saswali, wa chiwerewere, ndi kaafir ngati angafunikire madzi mumthawi yomwe alipo ochepa, tili ololedwa kusawasiira madzi ndi kupanga tayammamu chifukwa iwowa sali mugulu la zinthu zolemekezeka. Izi zikutiwonetsera kuwopsa kosiya swalah, kupanga chiwerewere ndi ukafir
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 17 · Mu malamulo a tayammum
⏱️ 30:30
“Gawo la mu malamulo a tayammamu, شُرُوطُ التَّيَمُّمِ:” Mulembi anatidziwitsa kuti malamulo amene akuyenera kukwiniritsidwa kuti tayammamu ikhale yokwanira pa Madh'hab a Shafi alipo 10;
  • Chopangira tayammamu chikhale dothi. Umu mukutuluka chilichonse chomwe si dothi.
  • Likhale dothi la twahara, loyera.
  • Dothilo lisakhale kuti lagwiritsidwa kale tchito ndi munthu wina popangira tayammamu. Madh'hab ena ngati a Hanabila ndi Malikiyyah amati izi zilibe vuto. Zomwe zili kufupi ndi chilungamo ndi zoti kugwiritsa tchito dothi loti wina wagwiritsa kale tchito popangira tayammamu zilibe vuto.
  • Dothilo lisasakanikirane ndi ufa ndi zomwe sizingagwiritsidwe tchito popangira tayammamu.
  • Munthu opanga tayammamuyo awunjike dothilo.
  • Munthu opanga tayammamu ayenera kupukuta ku khope ndi manja ake awiri poyika kapena komenya dothilo kawiri. Kumenya kamodzi dothi ndi kupukuta ku khope ndi mmanja momwe pa kumenya kumodziko, ndizololedwaso chifukwa Mtumiki ﷺ anapanga konso zimenezi.
  • Opanga tayammamu achotse kaye najsi pa thupi lake asanapange tayammamu.
  • Munthu asake kapena azindikire Qibra asanapange tayammamu. Izi ndi chifukwa choti munthu umafunika udzipanga tayammamu mthawi ya swalah ikalowa, ndi kuimika swalah pambuyo pomaliza tayammamu malingana ndi madh'hab a Shafi. Madh'hab ena ngati a Hanafi pa fundo iyi, amati munthu ukhoza kupanga tayammamu mthawi ina iliyonse. Izi ndi zomwe zili za mphavu kusiyana ndi zoyambazo.
  • Munthu adzipanga tayammamu mthawi ya Swalah ikalowa. Izi tafotokoza kale pa lamulo lachi 8.
  • Tayammamu adzipangidwa swalah ya Faradhwi ina iliyonse. Kutengera zomwe zili chifupi ndi chilungamo, zilibe vuto kupanga tayammamu ndikuswalira swalah za Faradhwi zingapo.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 18 · Zikakamizo pa tayammam | Zowononga tayammam
⏱️ 18:12
“Gawo la zomwe zili zachikakamizo pa tayammum, فِي فَرَائِضِ التَّيَمُّمِ:” Zithu zomwe zili za chikakamizo popanga tayammamu zilipo 5; 1.Kumenya dothi kapena kuika mmanja pa dothi 2. Chitsimikizo, Niyyah 3. Kupukuta kukhope 4. Kupukuta manja awiri 5. Kulondoloza pakati pa kupaka kuwiri. Kuyambira kukhope usanapange mmanja.
Zomwe zimaononga tayammamu zilipo zitatu;
  • Chilichonse chomwe chimawononga wudhu
  • Kutuluka chisilamu
  • Kupezeka kwa madzi ngati tayammamu anapangidwa kamba kakusowa kwa madzi. Ngati madzi apezeka tayammamu amawonongeka.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 19 · Zomwe zimayera kuchokera ku najsi | Mitundu ya Najsi
⏱️ 27:31
“Gawo la zomwe zimayera kuchokera ku najsi, فِيمَا يَطْهُرُ مِنَ النَّجَّاسَاتِ:” Zinthu zomwe zimayera kuchokera ku najsi, akuthauza kuti zithu zomwe zili najsi pazokha kenako ndi kukhala za twahara, zoyera. Izi zilipo zitatu;
  • Mowa ukapingidwa process yochotsedwa koledzeletsa pawokha. Ngati process yopangira vinegar.
  • Chikopa cha nyama yofa yokha chikapangidwa clean. Koma idzi ndi dzikopa dza nyama zomwe zimadyedwa zokha.
  • Chilichonse cha najsi chimene chimasanduka tidzilombo tamoyo. Mwachitsanzo, tidzilombo tomwe timatuluka mu nyama yoti yawola, patokha sitimakhala ta najsi.

Kusintha حَالَ condition ya chinthu kumathanso kupangitsa najsi kukhala ya twaahir kutengera Fiqh. Mwachitsanzo kugwiritsa tchito ndowe popanga manyowa. Izi zimasintha condition ya najsi ndipo kukathira kumunda sikungapangitse chomeracho kukhala cha najsi. “Gawo la mitundu ya najsi, أَقْسَامُ النَّجَاسَةِ:” Kudziwa mitundu ya najsi zimathandizira kudziwa kachotsedwe kake chifukwa ma najsi (unve) amasiyana kachotsedwe potengera kukula kwa najsi yo.
Mitundu ya najsi, kutengera makulidwe, ilipo itatu;
  • Yonkhwima kwambiri, الْمُغَلَّظَةٌ; Umu mumalowa najsi ya galu ndi nkhumba komanso chotuluka muzimenezi ngati nkodzo, chimbudzi ndi chobelekedwa kuchokera muzimenezi. Ngati galu or nkhumba ingakumane ndi chinyama china, chobelekedwa kuchokera mumkukumana kumeneku chimakhalaso najsi yayikulu.
  • Yopepuka, الْمُخَفَّفَةٌ; Umu muli nkodzo wa mwana wamwamuna amene sadayambe kudya zakudya zina kungopatula mkaka okha komanso sanakwanitse zaka ziwiri. Nkodzo uwu umakhala opepuka mukachotsedwe kake.
  • Yapakatikati, الْمُتَوَسِّطَةٌ; Ma najsi ena onse omwe sanatchuludwe mmagulu awiri a mmwambawa ngati mkodzo wa munthu, chimbudzi chamunthu ndi zinyama zodyedwa.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 20 · Kachotsedwe ka najsi
⏱️ 25:20
“Gawo la kachotsedwe ka najsi potengera kukula kwa najsi yo, فِي إِزَالَةِ النَّجَاسَةِ:” Najsi yomwe ndiyo nkhwima, الْمُغَلَّظَةٌ, imayera potsuka pa malo amene yagwera najsi po ka 7 pambuyo poyichotsa kaye najsi yo. Kamodzi mwa kutsuka ko, umayenera kutsukira mchenga.
Najsi yopepuka, الْمُخَفَّفَةٌ, imachotsedwa po waza madzi ochulukirapo kuposa najsi yo pamalo amene najsi yagwerapo. Kuchotsa ko kufike pa level yoti najsi sikuwonekaso ndi maso.
Najsi yomwe ndi yapakatikati, الْمُتَوَسِّطَةٌ, imachotsedwa mmagulu awiri;
  • Kutsoka najsi kwa الْعَيْنِيَّةُ; Uku ndi kuchotsa najsi ya mtundu, fungo ndi taste. Ngati najsi ndi ya mtundu, imayenera iyere mpaka mtundu ubwerere mmalo mwake. Chimodzimodzi ngati ndi ya fungo or taste umayenera kuyeretsa mpaka zimenezi zibwerere mchimake.
  • Kuchotsa najsi kwa الْحُكْمِيَّةُ; Uku ndi kuchotsa najsi imene yagwera pachinthu or pathupi koma sinasithe mtundu, fungo kapena taste. Kachotsedwe kake timatsukapo ndi madzi.

Izi zitithandize chifukwa anthu timasiya ku swali ndikupanga ma ibada ena chifukwa chosadziwa kachotsedwe ka ma najsi. Mwachitsanzo, nkodzo kukugwera penapake or umakodza nde sunapange istinjaa mthawi yomweyo sumakhala munthu okakamizika kusamba kuti uswali.
Kuduka twahara sichinthu chamasewera ngati mmene anthu timaganira.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 21 · Mu zokhudza haidhu ndi nifas
⏱️ 28:40
“Gawo la haidhu(kusamba-period) ndi nifas(kubereka/mtayo), فِي الْحَيْضِ وَ النِّفَاسِ:” Haidhu ndi kusamba kapena menstruation period. Masiku ochepa a haidhu ndi tsiku limodzi, ma ola 24, usiku ndi usana. Ndizotheka mzimayi kusamba kwa tsiku limodzi kwinako kukhala oyera. Koma azimayi ambiri amasamba pa masiku 6 kapena 7. Pamene maximum days yomwe mzimayi angapange period ndi masiku 15. Ngati mzimayi angadutsitse masiku 15, ameyenera kusamba ndi kuyamba kupanga ma ibada kapena zinthu zomwe zimakhala haram akakhala akupanga haidhu.
Pamene minimum period yakuyera, kutathauza kuti masiku amene mzimayi amakhala oyera pambuyo poti amasamba ndi masiku 15. Koma azimayi ambiri amapanga masiku 23 or 24. Kuyera kulibe maximum period, mzimayi amatha kukhala oyera podutsa masiku 24 wa.
Nifas ndi nyengo imene munthu wa mayi amakhala akutulutsa magazi pambuyo pobereka kapena mtayo. Magazi a nifas amatsimikizika pamene atuluka pambuyo poti mwana watuluka yense mmimba mwa mayi ake.
Nyengo yochepa ya nifas ndi kufwamphuka kwa magazi a nifas munthawi yomwe mwana wangotuluka. Magazi a period omwe amakaundana mchiberekero munthawi yomwe mzimayi ali oyembekezera, amatha kukakamizidwa ndi chiberekero kutuluka munthawi yomwe wangobereka.
Azimayi ambiri nyengo yawo ya nifas ndi masiku 40. Pamene maximum period ndi masiku 60 malingana ndi Madh'hab a Shafi. Madh'hab ena ngati a Malik ndi Hanabila komanso ma ulama ena aku madh'hab a Shafi amati maximum period ndi masiku 40. Ngati mzimayi angadutse masiku 40 akutulutsabe magazi, amatennga lamulo la istihaadhwa. Izi ndi zomwe zili chifupi ndi chilungamo.
Tidziwitsane kuti ngati magazi a nifas angasiye masiku 40 asanakwane, imakhala kuti nyengo ya nifas yatha, kotero mzimayi amayenera kudziyeretsa (kusamba) ndi kuyamba kupanga zomwe zinali haram pa iye.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 22 · Zifukwa zomwe zimamulora munthu kusiya swalah | Malamulo a swalah
⏱️ 30:00
“Gawo la zifukwa zomwe zimamulora munthu kusiya swalah kutathauza kuti mthawi ya swalah yonse kudutsa iyeyo osaswali, فِي أَعْذَارِ الصَّلَاةِ:” Zifukwa zomwe zili zovomelezeka kudutsitsa mthawi ya swalah yonse, osaswali mpaka kulowa mthawi ya swalah ina zilipo ziwiri;
  • Kugona, النَّوْمُ
  • Kuyiwala, النِّسْيَانُ

Kusiya swalah pa zifukwa zina osakhala ziwirizi, munthu amapeza tchimo.
Ngati munthu wagonereza kapena kuyiwaliza mpaka mthawi ya swalah yonse kudutsa, akadzuka kapena kukumbukira, aswali swalah yo mthawi yomweyo.
“Gawo la mu malamulo a swalah, فِي شُرُوطِ الصَّلَاةِ:” Malamulo a swalah alipo 8 koma tiyamba kuwona malamulo 5 kaye;
  • Kuziyeretsa ku malitsiro awiri, kukhala ndi twahara komanso wudhu
  • Kudziyeretsa ku najsi yomwe ili pa chovala chomwe munthu wavala kuti akaswali, pa thupi, ndi malo oswalira. Malo oswalira ndi okhawo amene thupi la munthu lidzipangira zonse za swalah.
  • Kubisa maliseche
  • Kuyang'ana ku Qibrah: Kwa amene ali ku Makkah ndi amene amafunika kuti adziyiyang'ana ka'aba ndendende. Amene ali kutali ndi ka'aba, amafunika kuti ayang'ane mbali yomwe kuli ka'aba yo. Sitikuyenera kudziika mu mchikakamizo choyang'ana ku Qibrah ndendende. Ngati sitikudziwa komwe kuli Qibrah, Mtumiki anati pakati pa kummawa ndi kumadzulo ndi komwe kuli Qibrah.
  • Kulowa kwa mthawi ya swalah: Lamulo ili ndi la mphanvu kwambiri kuposa malamulo ena. Kufikira poti mpaka ma Ulama ena anati ngati ulibe twahara ndipo mthawi ya swalah yatsala pang'ono kuti ithe, iweyo uswali opanda twahara. Kupanga adhana kapena kuswali mthawi yake isanalowe, ndi zosaloledwa.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 23 · Mu malamulo a swalah | Litsilo (Unve)
⏱️ 20:37
“Kupitiliza gawo la malamulo a swalah, فِي شُرُوطِ الصَّلَاةِ:”
  • Kuziyeretsa ku malitsiro awiri, kukhala ndi twahara komanso wudhu
  • Kudziyeretsa ku najsi yomwe ili pa chovala chomwe munthu wavala kuti akaswali, pa thupi, ndi malo oswalira.
  • Kubisa maliseche
  • Kuyang'ana ku Qibrah
  • Kulowa kwa mthawi ya swalah
  • Kukhala ndi uzindikiri wa uchikakamizo wa swalah
  • Munthu asakhale ndi chitsimikizo kuti chinthu cha faradhwi mu zinthu za faradhwi pa swalah ndi cha sunnah.
  • Kupewa zinthu zomwe zimawononga swalah

“Litsilo, الْأَحْدَاثُ:” Litsilo kapena unve ndi nyengo imene munthu akakhalamo imamulepheretsa iye kuswali. Unvewu uli mmagulu awiri;
  • Unve wawung'ono: Uwu ndi unve umene umapangitsa kuti kupanga wudhu kukhale kokamikizika pa munthu kuti aswale.
  • Unve wawukulu: Uwu ndi unve umene umapangitsa kusamba kukhala kokamikizika pa munthu kuti iye aswali.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 24 · Maliseche a Munthu
⏱️ 20:20
“Maliseche a munthu, الْعَوْرَاتُ:” Kubisa maliseche monga mmene tinawonera kuti ndi msichi imodzi ya swalah, Madh'hab a Shafi anatifotokozera kuti tiwadziwe maliseche komanso mmene tingabisire maliseche athu.
Madh'hab a Shafi anagawa maliseche a munthu mmitundu 4;
  • Maliseche a mwamuna aliyese ndi kapolo (slave) wachikazi pa swalah: Ndi zimene zili pakati pa nchombo ndi mabondo. Izi ziveke bwino kuti ngati munthu wapsinjika kuti ulibe kuthekera kovala zowonjera pamenepa, ukhoza kupanga choncho. Koma kuvala kodzilemekeza komanso motsatila sunnah ndizabwino kwambiri kwa msilamu.
  • Chisilamu chinawafewetsera azimayi omwe anali akapolo kumbali yakuvala chifukwa mthawi imeneyo kapolo amatengedwa ngati katundu wa bwana wake. Ndipo amakhala opanda chilichonse angakhale ndalama. Choncho Chisilamu chinawafewetsera akapolo kumbali ya zovala pa swalah chifukwa tonse ndi mboni kuti kuvala kumafuna ndalama.
  • Maliseche a mzimayi amene ndi mfulu pa swalah: Ndi thupi lake lonse kungopatula nkhope ndi zikhatho za manja.

  • Mzimayi akamaswali amayenera kuphimba thupi lake lonse kungopatula zikhatho za mmanja ndi nkhope. Izi ma ulama onse anagwirizana kuti zikuyenera kutero. Pomwe pali kusiyana pakati pa ma ulama ndi nkhani yophimba mapazi a mzimayi pa swalah.
    Madh'hab a Shafi ali mbali yoti mzimayi amphimbe mapazi ndipo sakuyenera kuwasiya mapazi adziwonekera pa swalah. Izi anavomeleza madh'hab a Malik ndi Hanbali komanso ma ulama ena. Pomwe madh'hab a Hanafi amati zabwino kwambiri ndi zoti mzimayi aswali ataphimba mapazi koma ngati angaswali osaphimba mapazi, swalah yake ndi yabwinobwino.
    Zabwino kwambiri kwa mzimayi ndi kuphimba mapazi pa swalah kuti akhale otetezeka ku zomwe ma ulama anasephana. Kuphimba mapazi, mzimayi akhoza kubisa ndi chovala chachitali kapena ma sokosi.
  • Maliseche a mzimayi amene ali mfulu ndi kapolo pa mwamuna amene akhoza kumukwatira: Ndi thupi lake lonse, kuvala niqaab.
  • Azimayi kubisa nkhope ndi zikhatho pa malo pomwe pali mwamuna amene akhoza kuwakwatira ndi nkhani inaso yomwe ma ulama anasiya. Madh'hab a Shafi anagonera kumbali yoti mzimayi akuyenera kuvala niqaab akakhala pamalo pomwe pali amuna oti akhoza kumukwatira. Madh'hab ena komanso ma ulama ena amati ndi sunnah mzimayi kuvala niqaab akakhala pamalo pomwe pali amuna oti akhoza kumukwatira.
  • Maliseche a mzimayi pamene ali ndi azibale ake komanso azimayi ena: Ndi zomwe zili pakati pa nchombo ndi mabondo.
  • Apanso ziveke bwino kuti mzimayi sakuyenera kupangira dala kumawawonetsa mabele abale ake. Koma ngati wachibale wachimuna atawona bele la mzimayi ngati pa mthawi yomwe akuyamwitsa ndi nyengo zina sipamakhala tchimo.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 25 · Msichi za Swalah
⏱️ 31:35
“Gawo la msichi za swalah, فِي أَرْكَانِ الصَّلَاةِ:” Msichi za swalah ndi zithu zimene zimayenera kukwaniritsidwa mu swalah ya munthu kuti swalah ya munthu yo ikhale yokwanira. Kusowekera kwa msichi imodzi pa swalah ya munthu kumasokoneza rakaa ya swalah ya munthuyo komanso swalah ya munthuyo imawonongekaa. Madh'hab a Shafi anazigawa msichi za swalah mmagulu 17 koma madh'hab ena anagawa kuti msichi za swalah zilipo 14;
  • Niyyah: Chitsimikizo
  • Takbeeratu al-ihram: Takbeera yotsegulira swalah yomwe ndi mawu woti "Allah Akbar". Ngati munthu angayambe swalah popanda kunena mawu woti Allah Akbar amakhala kuti swalah yo sanayambe ndipo akufunika kuti ayambireso. Tidziwitsaneso kuti msichi iyi ndi yomwe madh'hab ena komanso ma ulama ena anayiyika kuti msichi yoyambirira chifukwa swalah yamunthu imayamba ndi takbeera yotsegulira swalah. Pamene niyyah timapanga swalah isanayambike.
  • Kuyima kwa amene ali ndi kuthera kuswali choyima pa swalah ya faradhwi. Amene ali ndi kuthekera koswali choyima ali okakamizidwa kuswali choyima pa swalah ya faradwi. Pamene amene alibe kuthekera koswali choyima, akuyenera kuswali atakhala pansi kapena chogona. Swalah ya sunnah munthu akhoza kuswali chokhala angakhale alibe vuto linalililonse koma kuti amapeza half ya malipiro a swalah yo ngati itaswalidwa choyima. Akamati kuyima, uku ndi kuyima kosayadzamira chinachake kapena kudalira chinachilichonse.
  • Kuwerenga surat al-fatha: Ngati munthu akuswali ekha amayenera awerenge surat al-fatha. Koma ngati akuswali pa mbuyo pa imam mu swalah yokweza mawu ma ulama anasiyana, ena amati munthu awerengebe pamene ena amati asawerenge. Koma ngati munthu ukuswali wekha ndipo sunawerenge surat al-fatha, ndeti raka'a yo sinakwanire akuyenera abwerezenso. Izi zikutiwonetsera kuti ndi zokakamizika kuti Msilamu akuyenera kuphuzira kuwerenga surat al-fatha.
  • Kuwerama, ruku'u: Kuwerama komwe kuli kokwanira ndikuti munthu agwire mmabondo ndi zala zotayana. Ndipo nsana wake ukuyenera kukhala owongoka kufikira poti pa nsana po patayikidwa chinachake sichingatsetseleke mbali ina ya nsana wo. Komanso mutu wake ukuyenera kukhala pa level imodzi ndi nsana wake.
  • Kukhazikika pa ruku'u: Kukhazikika ndi kunena ma dhikr onse mokwanira monga subhana rabiya al-adhweemu, "سُبْحَانَ رَبّيَ الْعَظِيمِ".
  • Kuweramuka kuchoka pa ruku'u kupita pa Qauma: Kuyima mwa straight, mowongoka.
  • Kukhazikika pa qauma: Kukhala mokwanira bwinobwino.
  • Kupanga ma sajda awiri: Munthu akuyenera kupanga ma sajda onse awiri. Kusiya sajda imodzi, ndeti raka'a yo sinakwanire. Sajda yomwe ili yokwanira ndi kuti ziwalo 7 za munthu zigunde pansi:
    • Nkhope: Umu mumalowa chipumi ndi mphuno. Ziwirizi zimafunika zigunde pansi
    • Manja awiri: Umu mumalowa zikhatho zokha za manja onse awiri zokha basi.
    • mabondo awiri
    • Zala zamapazi awiri
    Komanso munthu sakuyenera kukhala modzifinya manja ake, koma akuyenera kuwatambasula ndi kupewa kuwaika manjaake pansi ngati mmene galu amakhalira akamapumula. Komanso akuyenera kugundanitsa mapazi ake ndi kupewa kuwaika mapazi ake mmwamba, kutathauza kuti mapazi ake adzigunda pansi.
  • Kukhazikika pa sajda: Kukhazikikapo ndi kupanga ma dhikr onse bwinobwino monga subhaana rabiya al-a'alaa "سُبْحَانَ رَبّيَ الْأَعْلَي"
  • Kukhala pakati pa ma sajda awiri
  • kukhazikika akakhala pakati pa ma sajda awiri: Kukhala ndikupanga ma dua onse mokwanira monga Allahuma ighfir lee warhamnee wahdinee wajburnee wa'afinee warzuqnee warfa'anee "اللّٰهُمَ اغْفِرْ لِى وَارْحَمْنِى وَاهْدِنِى وَاجْبُرْنِى وَعَافِنِى وَارْزُقْنِى وَارْفَعْنِى"ز
  • Kupanga tashahhud yomalizira: Kukhala pa tashahhud yomaliza yomwe timawerengera durood Ibraahim ndi kuperekera salaam. Swalah zonse za faradhwi zimakhala ndi ma tashahhud awiri kungopatula swalah ya fajr.
  • Kukhazikika pa tashahhud yomalizira: Munthu akuyenera kukhazikika pa tashahhud ndi kuwerenga attahiyaat yonse mokwanira bwino bwino kuti 'At-tahiyãtu lillähi was- salawatu wa-taiyibatu. As-Salamu alaika aiyuhan-Nabiyyu warahmatul-lãhi wa barakãtuhu. As-Salami 'alainã wa 'ala 'ibãdillah issalihin. Ash-hadu an lã-ilãha ill- Allahu wa ash-hadu anna Muhammadan 'abduhü wa Rasüluhu.' "التَّحِيَّاتُ لِلَّهِ وَالصَّلَوَاتُ وَالطَّيِّبَاتُ السَّلَامُ عَلَيْكَ أَيُّهَا النَّبِيُّ وَرَحْمَةُ اللَّهِ وَبَرَكَاتُهُ السَّلَامُ عَلَيْنَا وَعَلَى عِبَادِ اللّٰهِ الصَّالِحِينَ أَشْهَدُ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللّٰهُ وَأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا عَبْدُهُ وَرَسُولُهُ"
  • Kumufunira zabwino Mtumiki (SAAW): Kuwerenga durood Ibraahim pa tashahhud yomalizira ndi msichi ya swalah. Durood Ibrahim yomwe ili yokwanira ndi Allahuma swalli a'laa Muhammadin wa a'ala aali Muhammadin kamaa swallayta a'laa Ibrahim wa a'laa aali Ibraahim innaka hameedun majeedun. Allahuma baarik a'laa Muhammadin wa a'laa aali Muhammadin kamaa barakta a'alaa Ibraahim wa a'laa aali Ibrahim innaka hameedun majeedun. "اللّٰهُمَ صَلِّ عَلَى مُحَمَّدٍ وَعَلَى اَلِ مُحَمَّدٍ كَمَا صَلَّيْتَ عَلَى إِبْرَاهِيمَ وَعَلَى اَلِ إِبْرَاهِيمَ إِنَّكَ حَمِيدٌ مَّجِيدٌ اللّٰهُمَ بَارِكْ عَلَي مُحَمَّدٍ وَعَلَى اَلِ مُحَمَّدٍ كَمَا بَارَكْتَ عَلَي إِبْرَاهِيمَ وَعَلَى اَلِ إِبْرَاهِيمَ إِنَّكَ حَمِيدٌ مَّجِيدٌ".
  • Kupanda kuwerenga durood Ibraahim pa tashahhud yomalizira, swalah yo ndeti sinakwanire.
  • Kupereka salaam: Kupanga salaam kumanja ndiye msichi ya swalah pamene kupereka salaam kumazere ndi sunnah.
  • Kupanga mwa ndondomeko: Munthu akuyenera kupanga msichi za swalah zi mwa ndondomeko yake ndipo sakuyenera kuyambira cha pa tsogolo asanapange chapambuyo. Mwachitsanzo, sakuyenera kuyambira sajda asanapange ruku'u.
Tidziwitsaneso kuti swalah yonse munthu amafunika adzipanga zonse za pa swalah modekha ndi mokhazikika, osathamanga.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 26 · Niyyah ya pa swalah
⏱️ 22:59
“Gawo la mu niyyah ya pa swalah, فِي نِيَّهِ الصَّلَاةِ:” Niyyah ya pa swalah ndi chinthu chimodzi chomwe madh'hab a Shafi anachiyika kuti ndi msichi ya swalah. Mulembi anatifotokozera kuti tiyidziwe niyyah ya pa swalah.
Madh'hab a Shafi anayigawa niyyah ya pa swalah mu ma sitepe atatu potengera kuti ndi zinthu ziti zomwe zimayenera kupezeka mu niyyah ya munthu kuti ikhale yokwanira malingana ndi mtundu wa swalayo; 1. Swalah ya faradwi:
  • Ndi chikakamizo kuyika chitsimikizo cha kuswaliko
  • Asiyanitse swalah yo ku swalah zina za faradhwi
  • Kukhala ndi chitsimikizo kuti swalah yo ndi ya faradhwi, ya chikakamizo
2. Swalah ya sunnah ya padera, ya special: Swalah za sunnah za special zili mmagulu awiri; Zina zili ndi mthawi yake pomwe zina zimaswalidwa pa chifukwa chinachake. Mwachitsanzo, swalah za pambuyo ndi patsogolo pa swalah za faradhwi, swalah yopepha mvula kamba kakusowa kwa mvula, ndi swalah kukachitika kadamsana.
  • Ndi chikakamizo kuyika chitsimikizo cha kuswaliko
  • Asiyanitse swalah yo ku swalah zina za sunnah
3. Swalah ya sunnah yomwe siyapadera: Izi ndi swalah za sunnah zomwe zimaswalidwa opanda chifukwa chapadera komanso umatha kuswali mthawi ina iliyonse, kungopatula mu mthawi zomwe zili haram kuswali. Mwachitsanzo; swalah tikangolowa mu mzikiti (تَحِيَّةُ الْمَسْجِدِ) ndi Swalah yopepha chithandizo (صَلَاةُ الْإِسْتِخَارَةِ).
  • Mu swalah za sunnah iyi, ndi chikakamizo kuyika chitsimikizo cha kuswaliko basi

Mongowonjezera, mthawi zomwe zili haram kuswali sunnah ndi;
  • Mu mphindi zokwanira 15 mpaka 20 dzuwa likamatuluka mpaka lituluke dzuwa lonse
  • Masana dzuka likakhala pakatikati kuti tikuyandikira swalah ya dhuhur
  • Mu mphindi zimene dzuwa likulowa

Zivekeso bwino apa kuti niyyah zonsesi zimachitika mu mtima. Palibe kuyankhula ndi lilime tikamapanga niyyah ya pa swalah ina iliyonse angakhale tikamapanga ibada ina iliyonse.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 27 · Mu malamulo a Takbeeratu al-Ihram
⏱️ 34:32
“Gawo la mu malamulo a Takbeeratu yotsegulira swalah, فِي شُرُوطِ تَكْبِيرَةِ الْإِحْرَامِ:” Kudziwa za Takbeera yotsegulira swalah ndi chinthu chofunika kwambiri chifukwa Mtumiki ﷺ anati swalah imayamba ndi takbeeratu al-ihram. Kusiya osapanga kapena kunena takbeera yotsegulira swalah ndeti swalayo sinayambike. Choncho ndizofunika kuti msilamu adziwe bwino za takbeera yotsegulira swalah.
Malamulo a takbeera yotsegulira swalah alipo 16; 1. Idzinenedwa munthu atayima ngati ndi swalah ya faradhwi. Kungopatula munthu amene alibe kuthera koswali choyima. Pali mchitidwe umene anthu ochedwa amene akamajoina swalah imam ali pa ruku'u kapena ali malo ena osakhala pa Qiyam, amepezeka akunena takbeeratu al-ihram atawerama kapenanso akuyenda asanayime pa swaffa bwinobwino. Izi ndizofunika kupewa. 2. Takbeera inenedwe mu Arabic. Munthu adzinena mokwanira bwinobwino mu Arabic kuti "Allahu Akbar", اللّٰهُ أَكْبَرُ. 3. Mukhale mawu woti Allah. Munthu sakuyenera kusithanitsa mawu a 'Allah' ndi dzina lina la Allah ponena takbeera yotsegulira swalah. 4. Mukhale mawu woti Akbar. Apaso munthu asasithanitse mawu a 'Akbar' ndi mawu ena ofanana tathauzo ndi Akbar. 5. Mawu awiriwa atchulidwe mwa ndondomeko yake poyambira mawu woti Allah kumalizira Akbar. Munthu asayambire mawu woti Akbar ndi kumalizira a Allah. 6. Osakoka Hamza (ا) amene ali kumayambiriro kwa mawu woti Allah. Kukoka hamza yo, آ, kumasintha tathauzo chifukwa umakhala ngati ukufusa. 7. Osakoka ba (ب) wa pa mawu woti Akbar chifukwa kumasinthaso tathauzo. Kukoka ب kumapanga mawu a Akbar kupita ku Akbaar (أكبار) omwe amatathauza kuti ng'oma. Nde tikhoza kuwona mmene tathauzo likusinthira pamenepo. 8. Osayika shadda pa ba (ب). Izi anthu ena amazikonda ponena kuti AkBBar koma ndi zofunikanso kupewa chifukwa ukayika shadda umapanga mawu woti mu arabic mulibe. Nde ndi mawu opanda tathauzo. 9. Osawonjezera wawu (و) wa saakin kapena wawu wa haraka pakati pa mawu awiriwa. Mwachidule osakoka kumapeto kwa mawu woti Allah kuti Alla'huu' komanso osayika wawu wa fatha amene amalukizitsa mawu. 10. Osawonjezera wawu (و) kumbuyo kwa mawu woti Allah. Mwachidule osanena kuti Wallahu Akbar chifukwa wawu amalumikizitsa mawu. 11. Osayima kapena kupuma pakati pa mawu awiriwa, kuyima kwakutali kapena pang'ono. 12. Adzinvedwa mawu onse a takbeeratu al-ihraam ndi onenayo. Osanenera takbeeratu al-ihraam mu mtima. Lilime ndi milomo yathu idzigwedera ponena takbeeratu al-ihram chifukwa kunenera mumtima ndeti umakhala kuti ukuganiza sukuwerenga. Chimodzimodzi, pamalo ena aliwonse a swalah tidziwerenga moti lilime ndi milomo yathu idzigwedera. Ziveke bwino apa, osati kukweza mawu moti ena adzikunva, koma iweyo udzidziva wekha bwinobwino mawu onse a takbeeratu al-ihram. Kungopatula ngati uli Imam, ndeti ukweze kuti ena akunve. 13. Kulowa kwa mthawi ya swalayo. Takbeeratu al-ihraam adzinenedwa mthawi yake ya swalayo italowa. Munthu asapange takbeeratu al-hraam mthawi ya swalah isanalowe mkumati popeza ndikamamaliza swalayi ikhala mthawi yake yalowa. 14. Kupanga takbeeratu al-ihraam utayang'ana ku Qibra. 15. Munthu asalakwitse haroof ina iliyonse ya takbeeratu al-ihraam. Chilembo chilichonse chidzipatsidwa haqq yake kuti اللّٰهُ أَكْبَرُ. Kukwanitsa izi ndi zabwino kwambiri kumawerenga modekha, osapanga phuma. 16. Amene akupanga takbeeratu al-ihraam ali pambuyo pa imam, adzichedwetsa takbeera yakeyo podikira kuti imam apange kaye takbeera yake. Iye adzipanga takbeera yake pambuyo poti imam wamaliza kunena takbeera yake yonse. Amene angapange takbeeratu al-ihraam imam asanapange akufunika apangeso chifukwa imam anayikidwa kuti adzitsatidwa. Komanso Mtumiki anatilamula kupanga takbeera imam akapanga osati pamodzi naye kapena asapange.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 28 · Mu malamulo a surat al-Faatha
⏱️ 30:03
“Gawo la Mu malamulo a Surat al-Faatha, فِي شُرُوطِ الْفَاتِحَةِ.:” Pambuyo poona malamulo a takbeerat al-ihraam, chinamukomera mulembi kutipatsira malamulo omwe amayenera kukwaniritsidwa powerenga surat al-Faatha potengera kuti kuwerenga surat al-Faatha ndi imodzi mu msichi za swalah.
Surat al-Faatha yovomerezeka, ikuyenera kuwerengedwa motsatila malamulo ake. Kuphwanya kapena kuwononga malamulo amenewa kumawonga surat al-Faatha ndipo izi zimapangitsa kuti raka'a ya swalah yo iwonongeke.
Lamulo loyamba la Surat Al-Faatha ndi kulondoloza, kuwerenga mwa ndondomeko, التَّرْتِيْبُ. Surat al-Faatha ikuyenera kumawerengedwa mwa ndondomeko yake polondoloza ma ayah ake malingana ndi mmene anatsikira. Mwachitsanzo, sitikuyenera kuyambira kuwerenga verse yachitatu tisanawerenge verse yoyamba kapenaso kuwerenga verse yoyamba kenako ndikukawerenga verse ya chinayi. Kupanga izi kumawononga surat al-Faatha. Choncho mwanjira ina iliyonse, tikuyenera kumawerenga surat al-Faatha molondoloza ma ayah ake mu ndondomeko yake yoyenera.
Lamulo lina ndi kulumikizitsa ma ayah. Pambuyo poti tawerenga verse, tisamakhale mthawi yayitali tisanawerenge verse yotsatila ya surah al-Faatha. Komanso kusamalira dzilembo za surat al-Faatha pozitchula mmene zilili. Ndizoyenera kuti tidzitchula zilembo zomwe zili mu surat al-Faatha mmene zilili. Mwachitsanzo munthu asatchule ع mmalo mwa أ, kapenanso ح mmalo mwa ه, ndi zina zotero. Kulongosola izi, zikufunika munthu aphuzire kuwerenga Qur'an ndi tajweed yake molondola. Komanso, ndi zofunika kuti ife tidzibwerera ku zomwe tinaloweza kale kuti tidziwona ngati tikuwerenga surat al-Faatha mmene ilili potchula zilembo zake moyenerera.
Lamulo lina ndi kusamalira ma tashdeed (shadda) a Surat al-Faatha. Kumawonetsetsa powerenga Surat al-Faatha kuti mmalo onse amene ali ndi shadda tikutchula mokwanira chifukwa kusiyana shadda yo kumasitha tathauzo. Tisamakhale chete mthawi yayitali kapena yaying'ono tili ndi cholinga chodula kuwerenga surat al-Faatha. Surat al-Faatha ndi yoyenera kuti idziwerengedwa yonse ndipo munthu sakufunika adzidula surat al-Faatha. Kupanga izi kumawononga surat al-Faatha.
Lamulo lina pa madh'hab a Shafi ndi kuti ma ayah onse a surat al-Faatha adziwerengedwa wonse kuphatikiza Bismillah Rahmaan Raheem, بِسْمِ اللّٰهِ الرَّحْمٰنِ الرَّحِيمِ. Komanso tisamapange ma mistake omwe amasintha tathauzo powerenga. Tiwonetsetse kuti munkawerengedwe kathu ka surat al-Faatha sitikusokoneza mawu ake posintha kapena kusinthanitsa zilembo ndi ma haraka.
Lamulo lina ndi kuti munthu adziwerenga surat al-Faatha atayimilira pa swalah ya faradhwi. Tisaiwale kuti swalah za faradhwi ndi chikakamizo kuswali choyimilira kwa amene ali ndi kuthera koswali choyima. Kwa amene alibe kuthekera koswali choyima ndiwololedwa kuwerenga surat al-Faatha atakhala kapena chogona. Komanso tikamawerenga surat al-Faatha tidzidzinva tokha. Izi ndi chimodzimodzi zomwe tinafotokoza pa mthawi yomwe munthu akupanga takbeerat al-ihraam kuti lilime ndi milomo yathu idzigwedera tikamawerenga. Apaso ziveke bwino kuti osati mokweza mawu kuti ena adzikunva kungopatula ngati uli imam.
Lamulo lomalizira la surat al-Faatha ndi kuti asasakanize ndi chikumbo cha kunja kwa swalah. Munthu asalowetse kapena kuyankhula zinthu zina zomwe sizikugwirizana ndi zochitika za pa swalah, mthawi yomwe akuwerenga surah al-Faatha. Mwachitsanzo, imam akuwerenga bwino bwino ndee wina ndikudzangonena mawu ena mokweza. Izi zimatha kuwononga surat al-Faatha.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 29 · Ma Tashdeed a mu surat al-Faatha | Kunyamula manja pa mthawi imene tikupanga ma takbeera
⏱️ 19:37
“Gawo la mu ma Tashdeed a mu surat al-Faatha, فِي تَشْدِيدَاتِ الْفَاتِحَةِ. :” Malo amene ali ndi shadda mu surat al-Faatha alipo 14; 1. Pamwamba pa ل wa pa بِسْمِ اللّٰهِ. 2. Pamwamba pa ر wa pa الرَّحْمٰنِ. 3. Pamwamba pa ر wa pa الرَّحِيمِ. 4. Pamwamba pa ل wa pa mawu a Allah wa pa الْحَمْدُ لِلّٰهِ. 5. Pamwamba pa ب wa pa رَبِّ الْعَالَمِينَ. 6. Pamwamba pa ر wa pa الرَّحْمٰنِ. 7. Pamwamba pa ر wa pa الرَّحِيمِ. 8. Pamwamba pa د wa pa مٰلِكِ يَوْمِ الدِّينِ. 9. Pamwamba pa ي wa pa إِيَّاكَ نَعْبُدُ. 10. Pamwamba pa ي wa pa وَإِيَّاكَ نَسْتَعِينُ. 11. Pamwamba pa ص wa pa اهْدِنَا الصِّرٰطَ الْمُسْتَقِيمَ. 12. Pamwamba pa ل wa pa صِرٰطَ الَّذِينَ. 13. & 14. Pamwamba pa ض ndi ل wa pa أَنْعَمْتَ عَلَيْهِمْ غَيْرِ الْمَغْضُوبِ عَلَيْهِمْ وَلَا الضَّالِّينَ.
“Gawo la Kunyamula manja pa mthawi imene tikupanga ma takbeera, فِي رَفْعِ الْيَدَيْنِ عِنْدَ التَّكْبِيرِ:” Zili mu sunnah kukweza manja malo okwana 4 pa mthawi yomwe tikuswali:
  • Pa mthawi yomwe tikupanga takbeerat al-ihraam, takbeera yotsegulira swalah.
  • Pa mthawi yomwe tikupanga takbeera yopitila pa ruku'u.
  • Pa mthawi yomwe tikuweramuka kuchoka pa ruku'u.
  • Pa mthawi yomwe tikuyimilira kuchoka pa tashahhud yoyamba muswalah zomwe zili ndi ma raka'a opitilira awiri.

Zili mu sunnah kukweza manja pa swalah malo 4 amenewa okha basi. Kutathauza kuti, kukweza manja malo ena osakhala mmalo 4 awa si sunnah ya Mtumiki ﷺ, ndipo tiyenera kupewa kutero.
Mbali ina yofunikanso ndi kakwezedwe ka manja. Kakwezedwe komwe kali mu sunnah ndi kuyimika manja mpaka pa level ya makutu kapena pa level ya mapewa, zikhatho za mmanja kudziyang'anitsa ku Qibra. Ziveke bwino apa kuti level ya makutu osati kugwira ndi kukodola makutu kapena kudutsitsa makutu.
Chomalizira ndi kakwezedwe kabwino ndi kuti tidzikweza manja anthu pa mthawi imene tikupanga takbeera.
مَتْنُ سَفِيْنَةِ النَّجَاه Lesson 30 · Malamulo a Sajda
⏱️ 29:22
“Gawo la mu malamulo a sadja, فِي سُرُوطِ السُّجُودِ:” Sajda yokwanira mukuyenera kupeza zinthu 7 izi:
  • Sajda ichitike pa ziwalo 7, zikagunde pansi. Mtumiki (ﷺ) anati analamulidwa kuti ziwalo 7 zidzigunda pansi akamapanga sajda. Ngati ziwalo 7 sizinagunde pansi ndeti sajda yo sikukwanira.
  • Chipumi chamunthu chisaphimbidwe ndi chinachake. Chipumi chidzigunda malo opangira sajda wo direct.
  • Mutu udzikhazikika pa sajda. Osagwedezagwedeza mutu
  • Osapita pa sajda ndi chifukwa china kupatula chifukwa chopangira sajda.
  • Osayika ziwalo zomwe zimapita pa sajda pa chinthu chomwe chimasuntha chifukwa chakusuntha kwa ifeyo. Mwachitsanzo, osasanjikiza miyendo, komanso osasanjikiza manja, komanso osayika chipumi pamwamba pa manja.
  • Ziwalo za munsi zidzikhala mmwamba pamene mutu udzikwala pansi. Mwachidule, mutu wathu udzikhala pansi pamene zokhalira zathu zidzikhala mmwamba komanso osayika mutu pa chinthu ngati pillow. Tisapange sadja mofuna kufanananitsa level ya mutu wathu ndi zokhalira zathu. Aka nde kapangide kabwino ka sajda.
  • Kudekha; Tiyenera kupanga sajda yathu modekha.

“Gawo la ziwalo za pa sadja, فِي أَعْضَاءِ السُّجُودِ:” Ziwalo zomwe zimafunika kuti zidzigunda pansi popanga sajda zilipo 7:
  • 1. Chipumi; Chipumi ndi mphuno.
  • 2 & 3. Zikhatho za manja onse awiri
  • 4 & 5. Mabondo onse awiri
  • 6 & 7. Nkati kapena nsonga za zala zakumapanzi onse awiri